ANKANGOFUNA NTCHITO NANCY PART 1

ANKANGOFUNA NTCHITO NANCY PART 1

Dzina langa ndine nancy muthune ndakhala ndikufuna ntchito kwa nthawi yayitali almost kwa miyezi inayi kufikila nthawi imene ndinakafusila ntchito  pakampani ina yazomangamanga muzinda omwewu walilongwe.

mtafika kumaloko ndinakumana ndi oyang'anila anthu ogwira ntchito wakumeneko.tsiku loyamba kupitako kukampaniko adandiuza kuti kulibe malo akuti ndingingamagwireko ntchito nditamuchonderela kuti ntchito ndikuyifuna kwambiri anangoti ndipase nambala yako ya phone ndikuyimbira madzuro ano.

ndinabwerela kunyumba ndili osangalala ndichiyembekozo chakuti ntchito ndiipeza.

madzuro ake oyang'ana anaimbadi phone monga ananenela anandiuza kuti mawa ndimupeze mapalo ena odyera otchuka muno mumzinda wa lilongwe ndinali odabwa pang'ono kuti zitheka bwanji ntchito kukandipasila malo odyera koma poti ntchito ndinayifunitsitsa ndinangovomela kuti mmawa watsiku lotsatilaro ndimupeza kumalo tagwirizanawo.

mmawa kutacha ndinalawira kupita kukakumana ndi oyang'anila uja kumeneko anandigulira zakudya zabwino zabwino zambiri nditizakumwa tozizilitsa kukhosi then anandiuza tibayenda yenda kuongola miyendo.

ngakhale sindimkavetsetsa kuti munthuyi akusata ndondomeko zanji kuti andilembe ntchito ndimkangovomekezabe chilichose chimene wanena posafuna kumukhumudwisa kuti anganyanyale ntchitoyo osandilembanso.
 
titayenda pang'ono ankhota kumalo ena ogona alendo ndipo andiuza kuti watopa afuna akagoneko pang'ono kamba koti madzuro adzulo lake sanagone chifukwa ntchito inamuchulukila ndinamuvesetsa ndipo tinapita kumalo kuja kumene analipila room.imodzi yokha ndipo.tose tinakhala muchipinda chimodzi

to be continued.....

pangani follow pageyi πŸ‘‰πŸ‘‰ Collings Massinah    kuti pati 2 isakuphonyeni πŸ‘πŸ‘ NTCHITO NANCY PART 1

Comments

Popular posts from this blog

ZIONE PART 2😭😭

ZIONE PART 3